3 Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akuru a Israyeli anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengere likasa la cipangano la Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m'dzanja la adani athu.
4 Cifukwa cace anatumiza ku Silo kuti akatenge kumeneko likasalo la cipangano la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa akerubi; ndipo ana awiriwo a Eli, Hofeni ndi Pinehasi anali komweko ndi likasa la cipangano la Yehova.
5 Pakufika likasalo la cipangano la Yehova kuzithando, Aisrayeli onse anapfuula ndi mau okweza, kotero kuti dziko linacita cibvomezi.
6 Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kupfuula kwao, anati, Phokoso ili la kupfuula kwakukuru ku zithando za Aisrayeli litani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidzafika ku zithandozo.
7 Ndipo Afilisti anaopa, pakuti anati, Mulungu wafika kuzithando. Ndipo iwo anati, Tsoka kwa ife! popeza kale lonse panalibe cinthu cotere.
8 Tsoka kwa ife! adzatilanditsa ndani m'manja a milungu yamphamvu imeneyi? Milungu ija inakantha Aaigupto ndi masautso onse m'cipululu ndi yomweyi.
9 Limbikani, ndipo mucite camuna, Afilisti inu, kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga iwowa anali akapolo anu. Citani camuna nimuponyane nao.