3 Ndipo pakuuka a ku Asidodi mamawa, taonani Dagoni adagwa pansi, nagona cafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova. Ndipo iwo anatenga Dagoni namuimikanso m'malo mwace.
4 Ndipo m'mawa mwace polawirira, taonani, Dagoni adagwa pansi, nagona cafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova; ndipo mutu wace ndi zikhato zonse ziwiri za manja ace zinagona zoduka paciundo; Dagoni anatsala thupi lokha.
5 Cifukwa cace angakhale ansembe, angakhale ena akulowa m'nyumba ya Dagoni, palibe woponda pa ciundo ca Dagoni ku Asidodi, kufikira lero lino.
6 Koma Yehova anabvuta iwo a ku Asidodi ndi dzanja lace, nawaononga, nawazunza ndi mafundo, m'Asidodi ndi m'miraga yace.
7 Ndipo pamene anthu a ku Asidodi anaona kuti ncomweco, anati iwowa, Likasa la Mulungu wa Israyeli lisakhalitse ndi ife; popeza dzanja lace litiwawira ife, ndi Dagoni mulungu wathu.
8 Cifukwa cace anatumiza mithenga, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, nati, Ticite nalo ciani likasa la Mulungu wa Israyeli? Ndipo anati, Anyamule likasa la Mulungu kunka nalo ku Gati, Ndipo ananyamula likasalo la Mulungu wa Israyeli, napita nalo kumeneko.
9 Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mudziwo ndi kusautsa kwakukuru; ndipo anazunza anthu a mudziwo, akuru ndi ang'ono; ndi mafundo anawabuka.