6 Mulikuumitsiranji mitima yanu, monga Aaigupto ndi Farao anaumitsa mitima yao? Kodi iwo sana lola anthuwo amuke, iye atacita kodabwitsa pakati pao, ndipo anamuka?
7 Cifukwa cace tsono, tengani, nimukonze gareta latsopano, ndi ng'ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli cikhalire, ndipo mumange ng'ombezo pagareta, muzicotsere ana ao kunka nao kwanu;
8 ndipo mutenge likasa la Yehova, nimuliike pagaretapo; nimuike zokometsera zagolidi, zimene muzipereka kwa iye ngati nsembe yoparamula, m'bokosi pam bali pace; nimulitumize licoke.
9 Ndipo muyang'anire, ngati likwera pa njira ya malire ace ace ku Betisemesi, iye anaticitira coipa ici cacikuru; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, siliri lace; langotigwera tsokali.
10 Ndipo anthuwo anatero; natenga ng'ombe ziwiri zamkaka, nazimanga pagareta, natsekera anao kwao;
11 naika likasa la Yehova pagaretapo, ndi bokosi m'mene munali mbewa zagolidi ndi zifanizo za mafundo ao.
12 Ndipo ng'ombezo zinatsata njira yolunjika ku Betisemesi, niziyenda mumseu, zirikulira poyenda; sizinapambukira ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere; ndipo mafumu a Afilisti anazitsatira kufikira ku malire a Betisemesi.