3 Ndipo Samueli analankhula ndi banja lonse la Israyeli nati, Ngati mukuti mubwerere kunka kwa Yehova ndi mitima yanu yonse, cotsani pakati pa inu milungu yacilendo, ndi Asitaroti, nimukonzere Yehova mitima yanu, ndi kumtumikira iye yekha; mukatero, iye adzakupulumutsani m'manja a Afilisti.
4 Pomwepo ana a Israyeli anacotsa. Abaala ndi Asitaroti, natumikira Yehova yekha.
5 Ndipo Samueli anati, Musonkhanitse Aisrayeli onse ku Mizipa, ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.
6 Ndipo anaunjikana ku Mizipa, natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala cakudya tsiku lija, nati, Tinacimwira Yehova. Ndipo Samueli anaweruza ana a Israyeli m'Mizipa.
7 Ndipo pamene Afilisti anamva kuti Aisrayeli anasonkhana pamodzi ku Mizipa, mafumu a Afilisti anakwera kukayambana ndi Aisrayeli. Ndipo Aisrayeli pakumva ici, anacita mantha ndi Afilistiwo.
8 Ndipo ana a Israyeli anati kwa Samueli, Musaleke kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti iye atipulumutse m'manja a Afilistiwo.
9 Ndipo Samueli anatenga mwana wa nkhosa woyamwa, nampereka wathunthu kwa Yehova, nsembe yopsereza; ndipo Samueli anapempherera Israyeli kwa Yehova; ndipo Yehova anambvomereza.