8 Monga nchito zao zonse anazicita kuyambira tsiku lija ndinawaturutsa ku Aigupto, kufikira lero lino kuti anandisiya Ine, natumikira milungu yina, momwemo alikutero ndi iwenso.
9 Cifukwa cace tsono umvere mau ao koma uwacenjeze kolimba, ndi kuwadziwitsa makhalidwe ace a mfumu imene idzawaweruza.
10 Ndipo Samueli anauza anthu akumpempha iye mfumu mau onse a Yehova,
11 Nati, Awa ndi makhalidwe a mfumu imene idzaweruza inu; idzatenga ana anu amuna, akhale akusunga magareta, ndi akavale ace; ndipo adzathamanga ndi kutsogolera magareta ace;
12 idzawaika akhale otsogolera cikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yace, ndi kutema dzinthu zace, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magareta.
13 Ndipo idzatenga ana anu akazi apange zonunkhira, naphikire, naumbe mikate.
14 Ndipo idzalanda minda yanu, ndi minda yamphesa yanu, ndi minda yaazitona, inde minda yoposayo, nidzaipatsa anyamata ace.