12 Nayankha Eliya, nanena nao, Ndikakhala ine munthu wa Mulungu, utsike mota wakumwamba, nunyeketse iwe ndi makumi asanu ako. Pamenepo mota wa Mulungu unatsika kumwamba nunyeketsa iye ndi makumi asanu ace.
13 Ndipo anabwerezaaso kutuma mtsogolen wacitatu ndi makumi asanu ace. Nakwera mtsogoleri wacitatuyo, nadzagwada ndi maondo ace pamaso pa Eliya, nampembedza, nanena naye, Munthu wa Mulungu inu, ndikupemphani, moyo wanga ndi moyo wa anyamata anu makumi asanu awa akhale a mtengo wace pamaso panu.
14 Taonani, watsika mota wakumwamba, nunyeketsa atsogoleri awiri oyamba aja pamodzi ndi makumi asanu ao; koma tsopano moyo wanga ukhale wa mtengo wace pamaso panu.
15 Pamenepo mthenga wa Yehova anati kwa Eliya, Tsika naye, usamuopa. Nanyamuka iye, natsikira naye kwa mfumu.
16 Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israyeli kufunsira mau ace? Cifukwa cace sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.
17 Motero anafa monga mwa mau a Yehova adanena Eliyawo. Ndipo Yehoramu analowa ufumu m'malo mwace caka caciwiri ca Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, pakuti analibe mwana wamwamuna.
18 Macitidwe ace ena tsono adawacita Ahaziya, kodi salembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?