7 Ndipo kunali, powafika kalatayo, anatenga ana a mfumu, nawapha amuna makumi asanu ndi awiri, naika mitu yao m'mitanga, naitumiza kwa iye ku Yezreeli.
8 Nudza mthenga, numfotokozera, kuti, Abwera nayo mitu va ana a mfumu. Nati iye, Mulunjike miulu iwiri polowera pa cipata kufikira m'mawa.
9 Ndipo kunali m'ma wa, iye anaturuka, naima, nati kwa anthu onse, Muli olungama inu, taonani, ndinapandukira mbuye wanga ndi kumupha; koma awa onse anawakantha ndani?
10 Dziwani tsono, kuti sikadzagwa pansi kanthu ka mau a Yehova, amene Yehova ananena za nyumba va Ahabu; pakuti Yehova wacita cimene adanena mwa mtumiki wace Eliya.
11 Nawakantha Yehu otsala onse a nyumba ya Ahabu m'Yezreeli, ndi omveka ace onse, ndi odziwana naye, ndi ansembe ace, mpaka sanatsala wa iye ndi mmodzi yense.
12 Pamenepo ananyamuka, nacoka, namuka ku Samariya, Ndipo pokhala ku nyumba yosengera ya abusa panjira,
13 Yehu anakomana nao abale a Ahaziya mfumu ya Yuda, nati, Ndinu ayani? Nati iwo, Ife ndife abale a Ahaziya, tirikutsika kulankhulira ana a mfumu, ndi ana a nyumba yaikuru.