11 Macitidwe ena tsono a Zekariya, taonani, zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.
12 Awa ndi mau a Yehova anawanena ndi Yehu, ndi kuti, Ana ako kufikira mbadwo wacinai adzakhala pa mpando wacifumu wa Israyeli. Ndipo kunatero momwemo.
13 Salumu mwana wa Yabesi analowa ufumu wace caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai ca Uziya mfumu ya Yuda, nakhala mfumu mwezi umodzi m'Samariya.
14 Koma anakwera Menahemu mwana wa Gadi kucokera ku Tiriza, nafika ku Samariya, nakantha Salumu mwana wa Yabesi m'Samariya, namupha; nakhala mfumu m'malo mwace.
15 Macitidwe ena tsono a Salumu ndi ciwembu cace anacicita, taonani, zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.
16 Pamenepo Menahemu anakantha Tifisa, ndi onse anali m'mwemo, ndi malire ace kuyambira ku Tiriza; popeza sanamtsegulira pacipata; anaukantha, natumbula akazi onse a pakati okhala m'mwemo.
17 Caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai ca Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi analowa ufumu wace wa Israyeti, nakhala mfumu zaka khumi m'Samariya.