2 Anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka makumi asanu mphambu ziwiri m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu.
3 Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazicita atate wace Amaziya.
4 Komatu sanaicotsa misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.
5 Ndipo Yehova anadwaza mfumu, nakhala iye wakhate mpaka tsiku la imfa yace, nakhala m'nyumba ya padera. Ndipo Yotamu mwana wa mfumu anayang'anira banja la mfumu, naweruza anthu a m'dziko.
6 Macitidwe ena tsono a Azariya, ndi zonse anazicita, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?
7 Nagona Azariya ndi makolo ace, namuika ndi makolo ace m'mudzi wa Davide; nakhala mfumu m'malo mwace Yotamu mwana wace.
8 Caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu ca Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yerobiamu anakhala mfumu ya Israyeli m'Samariya miyezi isanu ndi umodzi.