6 Macitidwe ena tsono a Azariya, ndi zonse anazicita, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?
7 Nagona Azariya ndi makolo ace, namuika ndi makolo ace m'mudzi wa Davide; nakhala mfumu m'malo mwace Yotamu mwana wace.
8 Caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu ca Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yerobiamu anakhala mfumu ya Israyeli m'Samariya miyezi isanu ndi umodzi.
9 Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga adacita makolo ace; sanaleka zolakwa zace za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli.
10 Ndipo Salumu mwana wa Yabesi anamcitira ciwembu, namkantha pamaso pa anthu, namupha; nakhala mfumu m'malo mwace.
11 Macitidwe ena tsono a Zekariya, taonani, zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.
12 Awa ndi mau a Yehova anawanena ndi Yehu, ndi kuti, Ana ako kufikira mbadwo wacinai adzakhala pa mpando wacifumu wa Israyeli. Ndipo kunatero momwemo.