1 Caka cakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri ca Peka mwana wa Remaliya Ahazi mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda analowa ufumu wace.
2 Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi m'Yerusalemu; koma sanacita zoongoka pamaso pa Yehova Mulungu wace, ngati Davide kholo lace;
3 popeza anayenda m'njira ya mafumu a Israyeli, napititsanso mwana wace pamoto, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israyeli.
4 Ndipo anaphera nsembe, nafukiza zonunkhira kumisanje, ndi kuzitunda, ndi patsinde pa mtengo uli wonse wogudira.
5 Pamenepo Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israyeli, anakwera kumka ku Yerusalemu kukacita nkhondo, nammangira Ahazi misasa; koma sanakhoza kumgonjetsa.
6 Nthawi yomweyo Rezini mfumu ya Aramu anabwezera Elati kwa Aramu, napitikitsa Ayuda ku Elati; nadza Aaramu ku Elati, nakhala komweko kufikira lero lino.
7 Ndipo Ahazi anatuma mithenga kwa Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri, ndi kuti, Ine ndine kapolo wanu ndi mwana wanu; kwerani, mudzandipulumutse m'dzanja la mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la mfumu ya Israyeli anandiukirawo.