25 Ndipo kunali, poyamba iwo kukhala komweko, sanaopa Yehova; ndipo Yehova anawatumizira mikango, niwapha ena a iwowa.
26 Motero ananena ndi mfumu ya Asuri, kuti, Amitundu aja mudawacotsa kwao, ndi kuwakhalitsa m'midzi ya Samariya, sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli; cifukwa cace anawatumizira mikango pakati pao, ndipo taonani, irikuwapha; popeza sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli.
27 Pamenepo mfumu ya Asuri analamulira, kuti, Mukani naye komweko wina wa ansembe munawacotsako, nakakhale komweko, akawalangize makhalidwe a Mulungu wa dzikoli.
28 Nadza wina wa ansembewo adawacotsa ku Samariya, nakhala ku Beteli, nawalangiza m'mene azimuopera Yehova.
29 Koma a mtundu uli wonse anapanga milungu yao yao, naiika m'nyumba za misanje adazimanga Asamariya, a mtundu uli wonse m'midzi mwao mokhala iwo.
30 Ndipo anthu a Babulo anapanga Sukoti Bemoti, ndi anthu a Kuta anapanga Nerigali, ndi anthu a Hamati anapanga Asima,
31 ndi Aava anapanga Nibazi ndi Tarataka; ndi a Sefaravaimu anawatentha ana ao m'moto kwa Adrameleki, ndi Anameleki, milungu ya Asefaravaimu.