3 Pakuti anamanganso misanje, imene Hezekiya atate wace adaiononga; nautsira Baala maguwa a nsembe, nasema cifanizo, monga anacita Ahabu mfumu ya Israyeli, nagwadira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.
4 Namanga iye maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova imene Yehova adainenera kuti, M'Yerusalemu ndidzaika dzina langa.
5 Nalimangira khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.
6 Napititsa mwana wace pamoto, naombeza maula, nacita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anacita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wace.
7 Ndipo anaika cifanizo cosema cimene adacipanga m'nyumba ija Yehova adainenera kwa Davide ndi kwa Solomo mwana wace kuti, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha mwa mafuko onse a Israyeli ndidzaikamo dzina langa kosatha.
8 Ndipo sindidzacotsanso mapazi a Israyeli m'dziko ndidalipereka kwa makolo ao; cokhaci asamalire kucita monga mwa zonse ndawalamulira ndi monga mwa cilamulo conse anawalamulira Mose mtumiki wanga.
9 Koma sanamvera, nawalakwitsa Manase, nawacititsa coipa, kuposa amitundu amene Yehova adawaononga pamaso pa ana a Israyeli.