5 Ndipo kunatero, atatha masiku a madyererowa Yobu anatumiza mau, nawapatula, nauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuwerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anacimwa ana anga, nacitira Mulungu mwano m'mtima mwao. Anatero Yobu masiku onse.
6 Ndipo panali tsiku lakuti ana a Mulungu anadza kudzionetsa kwa Yehova, nadzanso Satana pakati pao.
7 Nati Yehova kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana kwa Yehova, nati, Kupitapita m'dziko ndi kuyendayenda m'mwemo.
8 Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? pakuti palibe wina wonga iye m'dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.
9 Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kodi Yobu aopa Mulungu pacabe?
10 Kodi simunamcinga iye ndi nyumba yace, ndi zace zonse, pomzinga ponse? nchito ya manja ace mwaidalitsa, ndi zoweta zace zacuruka m'dziko.
11 Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zace zonse, ndipo adzakucitirani mwano pankhope panu.