10 Analembera madziwo malire,Mpaka polekeza kuunika ndi mdima.
11 Mizati ya thambo injenjemera,Ndi kudabwa pa kudzudzula kwace.
12 Mwa mphamvu yace agwetsa nyanja bata;Ndipo mwa luntha lace akantha kudzikuza kwace.
13 Mwa mzimu wace anyezimiritsa thambo;Dzanja lace linapyoza njoka yothawayo.
14 Taonani, awa ndi malekezero a njira zace;Ndi cimene tikumva za Iye ndi cinong'onezo cacing'ono;Koma kugunda kwa mphamvu yace akuzindikiritsa ndani?