1 Ndipo Yobu anaonjezanso mwambi wace, nati,
2 Pali Mulungu, amene anandicotsera zoyenera ine,Ndi Wamphamvuyonse, amene anawawitsa moyo wanga,
3 Pakuti moyo wanga wonse ukali mwa ine,Ndi mpweya wa Mulungu m'mphuno mwanga;
4 Milomo yanga siilankhula cosalungama,Ndi lilime langa silichula zacinyengo.
5 Sindibvomereza konse kuti muli olungama;Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.
6 Ndiumirira cilungamo canga, osacileka;Cikhalire moyo ine, mtima wanga sunditonza.