1 Koma tsopano iwo osafikana msinkhu wanga andiseka,Iwo amene atate ao ndikadawapeputsa, osawaika pamodzi ndi agaru olinda nkhosa zanga.
2 Mphamvunso ya m'manja mwao ndikadapindulanji nayo?Ndiwo anthu amene unyamata wao udatha,
3 Atsala mafupa okha okha ndi kusowa ndi njala;Akungudza nthaka youma kuli mdima wa m'cipululu copasuka.
4 Achera terere lokolera kuzitsamba,Ndi cakudya cao ndico mizu ya dinde.
5 Anawapitikitsa pakati pa anthu,Awapfuulira ngati kutsata mbala.
6 Azikhala m'zigwa za cizirezire,M'maenje a m'nthaka ndi m'mapanga.
7 Pakati pa zitsamba alira ngati buru,Pansi pa khwisa asonkhana pamodzi.