8 Ndipo tsono, mudzitengere ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu, mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu, pakuti ndidzambvomereza iyeyu, kuti ndisacite nanu monga mwa kupusa kwanu; popeza simunandinenera coyenera monga ananena mtumiki Yobu.
9 Namuka Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofara wa ku Naama, nacita monga Yehova adawauza; ndipo Yehova anabvomereza Yobu.
10 Ndipo Yehova anacotsa ukapolo wa Yobu, pamene anapempherera mabwenzi ace; Yehova nacurukitsa zace zonse za Yobu mpaka kuziwirikiza.
11 Pamenepo anamdzera abale ace onse, ndi alongo ace onse, ndi onse odziwana naye kale, nadya naye mkate m'nyumba yace, nampukusira mitu, namtonthoza pa zoipa zonse Yehova anamfikitsirazi; nampatsanso yense ndarama ndi mphete yagolidi.
12 Ndipo Yehova anadalitsa citsiriziro ca Yobu koposa ciyambi cace, ndipo anali nazo nkhosa zikwi khumi ndi zinai, ndi ngamila zikwi zisanu ndi cimodzi, ndi ng'ombe zamagoli cikwi cimodzi, ndi aburu akazi cikwi cimodzi.
13 Anali naonso ana amuna asanu ndi awiri ndi ana akazi atatu.
14 Ndipo anamucha dzina la woyamba Yemima, ndi dzina la waciwiri Keziya, ndi dzina la wacitatu Kerenihapuki.