8 Ndipo iye anati, Yang'anirani musasoceretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao.
9 Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi mapanduko, musaopsedwa; pakuti ziyenera izi ziyambe kucitika; koma mathedwe sakhala pomwepo.
10 Pamenepo ananena nao, Mtundu wa anthu udzaukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina:
11 ndipo kudzakhala zibvomezi zazikuru, ndi njala ndi miliri m'malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zoopsya ndi zizindikilo zazikuru zakumwamba.
12 Koma zisanacitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, cifukwa ca dzina langa.
13 Kudzakhala kwa inu ngati umboni.
14 Cifukwa cace tsimikizani mumtima mwanu, kuti usanafike mlandu musalingirire cimene mudzayankha.