10 koma m'mene analikumkonzera cakudya kudamgwera ngati kukomoka;
11 ndipo anaona pathambo padatseguka, ndi cotengera cirinkutsika, conga ngati cinsaru cacikuru, cogwiridwa pa ngondya zace zinai, ndi kutsikira padziko pansi;
12 m'menemo munali nyama za miyendo inai za mitundu yonse, ndi zokwawa za padziko ndi mbalame za m'mlengalenga.
13 Ndipo anamdzera mau, Tauka, Petro; ipha, nudye.
14 Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadya ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa.
15 Ndipo mau anamdzeranso nthawi yaciwiri, Cimene Mulungu anayeretsa, usaciyesa cinthu wamba.
16 Ndipo cinacitika katatu ici; ndipo pomwepo cotengeraco cinatengedwa kunka kumwamba.