2 Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala cakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Bamaba ndi Saulo ku nchito imene odinawaitanirako.
3 Pamenepo, m'mene adasala cakudya ndi kupemphera ndi kuika manja pa iwo, anawatumiza amuke.
4 Pamenepo iwo, otumidwa ndi Mzimu Woyera, anatsikira ku Selukeya; ndipo pocokerapo anapita m'ngalawa ku Kupro.
5 Ndipo pokhala ku Salami, analalikira mau a Mulungu m'masunagoge a Ayuda; ndipo anali nayenso Yohane mnyamata wao.
6 Ndipo m'mene anapitirira cisumbu conse kufikira Pafo, anapezapo munthu watsenga, mneneri wonyenga, ndiye Myuda, dzina lace Baryesu;
7 ameneyo anali ndi kazembe Sergio Paulo, ndiye munthu wanzeru. Yemweyo anaitana Barnaba ndi Saulo, nafunitsa kumva mau a Mulungu.
8 Koma Elima watsengayo (pakuti dzina lace litera posandulika) anawakaniza, nayesa kupatutsa kazembe asakhulupire.