16 Ndipo panali, pamene tinalinkunka kukapemphera, anakomana ndi ife namwali wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ace zambiri pakubwebweta pace.
17 Ameneyo anatsata Paulo ndi ite, napfuula, kuti, Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba amene akulalikirani inu njira ya cipulumutso.
18 Ndipo anacita cotero masiku ambiri. Koma Paulo anabvutika mtima ndithu, naceuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Kristu, turuka mwa iye. Ndipo unaturuka nthawi yomweyo.
19 Koma pamene ambuye ace anaona kuti kulingalira kwa kupindula kwao kwatha, anagwira Paulo ndi Sila, nawakokera kunka nao kubwalo kwa akuru,
20 ndipo pamene adanka nao kwa oweruza, anati, Anthu awa abvuta kwambiri mudzi wathu, ndiwo Ayuda,
21 ndipo alalikira miyambo imene siiloleka ife kuilandira, kapena kuicita, ndife Aroma.
22 Ndipo linagumukira iwo khamulo; ndipo oweruza anawang'ambira maraya ao; nalamulira kuti awakwapule.