30 nawaturutsira iwo kunja, nati, Ambuye, ndicitenji kuti ndipulumuke?
31 Ndipo iwo anati, Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako.
32 Ndipo anamuuza iye mau a Ambuye, pamodzi ndi onse a pabanja pace.
33 Ndipo anawatenga ora lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yao; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pace.
34 Ndipo anakwera nao kunka kunyumba kwace, nawakhazikira cakudya, nasangalala kwambiri, pamodzi ndi a pabanja pace, atakhulupirira Mulungu.
35 Kutaca, oweruza anatumiza akapitao, kuti, Mukamasule anthu aja.
36 Ndipo mdindo anafotokozera mauwo kwa Paulo, nati, Oweruza atumiza mau kunena kuti mumuke; tsopanotu turukani, mukani mumtendere.