1 Pamene anapitirira pa Amfipoli, ndi Apoloniya, anafika ku Tesalonika, kumene kunali sunagoge wa Ayuda.
2 Ndipo Paulo, monga amacita, analowa kwa iwo; ndipo masabata atatu ananena ndi iwo za m'malembo, natanthauzira,
3 natsimikiza, kuti kunayenera Kristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Kristu.
4 Ndipo ena a iwo anakopedwa, nadziphatika kwa Paulo ndi Sila; ndi Ahelene akupembedza aunyinji ndithu, ndi akazi akuru osati owerengeka.
5 Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa acabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nacititsa phokoso m'mudzi; ndipo anagumukira ku nyumba ya Yasoni, nafuna kuwaturutsira kwa anthu.
6 Pamene sanawapeza anakokera Yasoni ndi abale ena pamaso pa akuru a mudzi, napfuula kuti, Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso;
7 amene Yasoni walandira; ndipo onsewo acita zokana malamulo a Kaisara; nanena kuti pali mfumu yina, Yesu.