24 Ndipo anafika ku Efeso Myuda wina dzina lace Apolo, pfuko lace la ku Alesandreya, munthu wolankhula mwanzeru; ndipo anali wamphamvu m'malembo.
25 Iyeyo aoaphunzitsidwa m'njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wacangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha;
26 ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m'sunagoge, koma pamene anamumva iye Priskila ndi Akula, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.
27 Ndipo pamene iye anafuna kuoloka kunka ku Akaya, abale anamfulumiza, ndi kulembera akalata kwa akuphunzira kuti amlandire: ndipo pamene anafika, iye anathangata ndithu iwo akukhulupira mwa cisomo;
28 pakuti ndi mphamvu anatsutsa Ayuda, pamaso pa anthu, nasonyeza mwa malembo kuti Yesu ndiye Kristu.