26 Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja:
27 ndipo tiopa ife kuti nchito yathuyi idzayamba kunyonyosoka; komanso kuti kacisi wa mlungu wamkazi Artemi adzayamba kuyesedwa wacabe; ndiponso kuti iye adzayamba kutsitsidwa ku ukulu wace, iye amene a m'Asiya onse, ndi onse a m'dziko lokhalamo anthu, ampembedza.
28 Ndipo pamene anamva, anadzala ndi mkwiyo, napfuula, nati, Wamkuru ndi Artemi wa ku Efeso,
29 Ndipo m'mudzi monse munacita piringu-piringu, nathamangira onse pamodzi ku bwalo losewera, atagwira Gayo ndi Aristarko, anthu a ku Makedoniya, alendo anzace a Paulo.
30 Ndipo pamene Paulo anafuna kulowa kwa anthu, akuphunzira ace sanamloleza.
31 Ndipo akulu ena a Asiyanso, popeza anali abwenzi ace, anatumiza mau kwa iye, nampempha asadziponye ku bwalo lakusewera.
32 Ndipo ena anapfuula kanthu kena, ena kanthu kena; pakuti msonkhanowo unasokonezeka; ndipo unyinji sunadziwa cifukwa cace ca kusonkhana.