16 komatu ici ndi cimene cinanenedwa ndi mneneri Yoeli,
17 Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu,Ndidzathira ca Mzimu wansa pa thupi liri lonse,Ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera,Ndipo anyamata anu adzaona masomphenya,Ndi akulu anu adzalota maloto;
18 Ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m'masiku awaNdidzathira ca Mzimu wanga; ndipo adzanenera.
19 Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m'thambo la kumwamba,Ndi zizindikilo pa dziko lapansi;Mwazi, ndi moto, ndi mpweya wautsi;
20 Dzuwa lidzasanduka mdima,Ndi mweziudzasanduka mwazi,Lisanadze tsiku la Ambuye,Lalikuru ndi loonekera;
21 Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina laAmbuye adzapulumutsidwa.
22 Amuna inu Aisrayeli, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wocokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndizimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikilo, zimene Mulungu anazicita mwa iye pakati pa inu, monga mudziwa nokha;