4 Ndipo anamperekeza kufikira ku Asiya Sopatro mwana wa Puro, wa ku Bereya; ndipo Atesalonika, Aristarko ndi Sekundo; ndi Gayo wa ku Derbe, ndi Timoteo; ndi a ku Asiya, Tukiko ndi Trofimo.
5 Koma iwowa adatitsogolera, natilinda ku Trowa.
6 Ndipo tinapita m'ngalawa kucokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda cotupitsa, ndipo popita masiku asanu tinawapeza ku Trowa; pamenepo tinatsotsa masiku asanu ndi awiri.
7 Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati acoke m'mawa mwace; ndipo ananena cinenere kufikira pakati pa usiku.
8 Ndipo munali nyali zambiri m'cipinda ca pamwamba m'mene tinasonkhanamo.
9 Ndipo mnyamata dzina lace Utiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikuru; ndipo pakukhala cifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja paciwiri, ndipo anamtola wakufa.
10 Ndipo potsikirako Paulo, anamgwera namfungatira, nati, Musacite phokoso, pakuti moyo wace ulipo.