7 Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati acoke m'mawa mwace; ndipo ananena cinenere kufikira pakati pa usiku.
8 Ndipo munali nyali zambiri m'cipinda ca pamwamba m'mene tinasonkhanamo.
9 Ndipo mnyamata dzina lace Utiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikuru; ndipo pakukhala cifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja paciwiri, ndipo anamtola wakufa.
10 Ndipo potsikirako Paulo, anamgwera namfungatira, nati, Musacite phokoso, pakuti moyo wace ulipo.
11 Ndipo m'mene adakwera, nanyema mkate, nadya, nakamba nao nthawi, kufikira kuca, anacokapo,
12 Ndipo anadza naye mnyamata ali wamoyo, natonthozedwa kwakukuru.
13 Koma ife tinatsogolera kunka kungalawa, ndipo tinapita ku Aso, pamenepo tinati timlandire Paulo; pakuti anatipangira comweco, koma anati ayenda pamtunda yekha.