1 Amuna, abale, ndi atate, mverani codzikanira canga tsopano, ca kwa inu.
2 Ndipo pakumva kuti analankhula nao m'cinenedwe ca Cihebri, anaposa kukhala cete; ndipo anati:
3 ine ndine munthu Myuda, wobadwa m'Tariso wa Kilikiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliyeli, wolangizidwa monga mwa citsatidwe ceni ceni ca cilamulo ca makolo athu, ndipo ndinali wacangu, colinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero;
4 ndipo ndinalondalonda Njira iyi kufikira imfa, ndi kumanga ndi kupereka kundende amuna ndi akazi.
5 Monganso mkulu wa ansembe andicitira umboni, ndi bwalo lonse la akuru; kwa iwo amenenso ndinalandira akalata kunka nao kwa abale, ndipo ndinapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nao omangidwa ku Yerusalemu, kuti alangidwe.
6 Ndipo kunali, pakupita ine ndi kuyandikira ku Damasiko, monga usana, mwadzidzidzi kunandiwalira pondizungulira ine kuunika kwakukuru kocokera kumwamba.