13 anadza kwa ine, ndipo poimirirapo anati kwa ine, Saulo, mbale, penyanso. Ndipo ine, ora lomweli ndinampenya.
14 Ndipo anati, Mulungu wa makolo athu anakusankhiratu udziwe cifuniro cace, nuone Wolungamayo, numve mau oturuka m'kamwa mwace.
15 Ndipo udzamkhalira iye mboni kwa anthu onse, za izo udaziona ndi kuzimva.
16 Ndipo tsopano ucedweranji? Tauka, nubatizidwe ndi kusamba kucotsa macimo ako, nuitane pa dzina lace.
17 Ndipo kunali, nditabwera ku Yerusalemu ndinalikupemphera m'Kacisi, ndinacita ngati kukomoka,
18 ndipo ndinamuona iye, nanena nane, Fulumira, turuka msanga m'Yerusalemu; popeza sadzalandira umboni wako wakunena za Ine.
19 Ndipo ndinati ine, Ambuye, adziwa iwo okha kuti ndinali kuika m'ndende ndi kuwapanda m'masunagoge onse iwo akukhulupirira Inu;