27 Ndipo kapitao wamkuruyo anadza, nati kwa iye, Ndiuze, iwe ndiwe Mroma kodi? Ndipo anati, Inde.
28 Ndipo kapitao wamkuru anayankha, Ine ndalandira ufulu umene ndi kuperekapo mtengo wace waukuru. Ndipo Paulo anati, Koma ine ndabadwa Mroma.
29 Pamenepo ndipo iwo amene anati amfunsefunse, anamsiya; ndipo kapitao wamkurunso anaopa, pozindikira kuti ndiye Mroma, ndiponso popeza adammanga iye.
30 Koma m'mawa mwace pofuna kuzindikira cifukwa cace ceni ceni cakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe akulu, ndi bwalo lonse la akulu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao.