13 ndipo iwo amene adacita cilumbiro ici anali oposa makumi anai.
14 Amenewo anadza kwa ansembe akulu ndi akulu, nati, Tadzitemberera nalo temberero kuti sitidzalawa kanthu kufikira titamupha Paulo.
15 Potero tsopano inu ndi bwalo la akuru muzindikiritse kapitao wamkuru kuti atsikenaye kwa inu, monga ngati mufuna kudziwitsitsa bwino za iye; koma tadzikonzeratu timuphe asanayandikire iye.
16 Koma mwana wa mlongo wace wa Paulo anamva za cifwamba cao, ndipo anadza nalowa m'linga, namfotokozera Paulo.
17 Ndipo Paulo anadziitanira kenturiyo wina, nati, Pita naye mnyamata uyu kwa kapitao wamkuru; pakuti ali nako kanthu kakumfotokozera iye.
18 Pamenepo ndipo anamtenga, napita naye kwa kapitao wamkuru, nati, Wam'nsingayo Paulo anandiitana, nandipempha ndidze naye mnyamata uyu kwa inu, ali nako kanthu kakulankhula ndi inu.
19 Ndipo kapitao wamkuru anamgwira dzanja, napita naye padera, namfunsa m'tseri, Ciani ici uli naco kundifotokozera?