12 Pamenepo Festo, atakamba ndi aphungu ace, anayankha, Wanena, Ndirurukira kwa Kaisara; kwa Kaisara udzapita.
13 Ndipo atapita masiku ena, Agripa mfumuyo, ndi Bemike anafika ku Kaisareya, nalankhula Festo.
14 Ndipo atatsotsako masiku ambiri, Festo anafotokozera mfumuyo mlandu wace wa Paulo, nanena, Pali munthu adamsiya m'ndende Felike,
15 amene ansembe akulu ndi akulu a Ayuda anamnenera kwa ine, ndiri ku Yerusalemu, nandipempha ndiipitse mlandu wace.
16 Koma ndinawayankha, kuti macitidwe a Aroma satero, kupereka munthu asanayambe woneneredwayo kupenyana nao omnenera ndi kukhala napo podzikanira pa comneneraco.
17 Potero, pamene adasonkhana pano, sindinacedwa, koma m'mawa mwace ndinakhala pa mpando waciweruziro, ndipo ndinalamulira adze naye munthuyo.
18 Ndipo pamene anaimirira omneneza, sanamchulira konse cifukwa ca zoipa zonga ndinazilingirira ine;