13 Ndipo poomba pang'ono mwela, poyesa kuti anaona cofunirako, anakoka nangula, napita m'mbali mwa Krete.
14 Koma patapita pang'ono idaombetsa kucokerako mphepo ya namondwe, yonenedwa Eurokulo;
15 ndipo pogwidwa nayo ngalawa, yosakhoza kupitanso mokomana nayo mphepo, tidangoleka, ndipo tinangotengedwa.
16 Ndipo popita kutseri kwa cisumbu cacing'ono dzina lace Kauda, tinakhoza kumangitsa bwato koma mobvutika;
17 ndipo m'mene adaukweza, anacita nazo zothandizira, nakulunga ngalawa; ndipo pakuopa kuti angatayike pa Surti, anatsitsa matanga, natengedwa motero.
18 Ndipo pobvutika kwakukuru ndi namondweyo, m'mawa mwace anayamba kutaya akatundu;
19 ndipo tsiku lacitatu anataya ndi manja ao a iwo eni zipangizo za ngalawa.