4 Koma ife tidzalimbika m'kupemphera, ndi kutumikira mau.
5 Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi cikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanora ndi Timo, ndi Parmena, ndi Nikolao, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya:
6 amenewo anawaika pamasopa atumwi; ndipo m'mene adapemphera, anaika manja pa iwo.
7 Ndipo mau a Mulungu anakula; ndipo ciwerengero ca akuphunzira cidacurukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikuru la ansembe linamvera cikhulupiriroco.
8 Ndipo Stefano, wodzala ndi cisomo ndi mphamvu, anacita zozizwa ndi zizindikilo zazikuru mwa anthu.
9 Koma anauka ena a iwo ocokera m'sunagoge wa Alibertino, ndi Akurenayo, ndi Aalesandreyo, ndi mwa iwo a ku Kilikiya ndi ku Asiya, natsutsana ndi Stefano.
10 Ndipo sanathe kuilaka nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.