8 Ndipo Stefano, wodzala ndi cisomo ndi mphamvu, anacita zozizwa ndi zizindikilo zazikuru mwa anthu.
9 Koma anauka ena a iwo ocokera m'sunagoge wa Alibertino, ndi Akurenayo, ndi Aalesandreyo, ndi mwa iwo a ku Kilikiya ndi ku Asiya, natsutsana ndi Stefano.
10 Ndipo sanathe kuilaka nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.
11 Pamenepo anafuna anthu akumpitira pansi, ndi kuti, Tidamumva iye alikunenera Mose ndi Mulungu mau amwano.
12 Ndipo anautsa anthu, ndi akuru, ndi alembi, namfikira, namgwira iye, nadza naye ku bwalo la akulu,
13 naimika mboni zonama, zakunena, Munthu ameneyo saleka kunenera malo oyera amene, ndi cilamulo;
14 pakuu tinamumva iye alikunena, kuti, Yesu Mnazarayo amene adzaononga malo ano, nadzasanduliza miyambo imene Mose anatipatsa.