1 Ndipo Saulo analikubvomerezana nao pa imfa yace. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukuru pa Mpingo unali m'Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi samariya, koma osati atumwi ai.
2 Ndipo anamuika Stefano anthu opembedza, namlira maliro akuru.
3 Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa m'nyumba m'nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m'ndende.
4 Pamenepo ndipo iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mauwo.
5 Ndipo Filipo anatsikira ku mudzi wa ku Samarlya, nawalalikira iwo Kristu.