8 Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ace, sanapenya kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye ni'Damasiko.
9 Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadya kapena kumwa.
10 Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lace Hananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Hananiya. Ndipo anati, Ndiri pano, Ambuye,
11 Ndipo Ambuye anati kwa iye, Tauka, pita ku khwalala lochedwa Lolunjika, ndipo m'nyumba ya Yuda ufunse za munthu dzina lace Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera
12 ndipo anaona mwamuna dzina, lace Hananiya, alikulowa, namuika manja, kuti apenyenso.
13 Ndipo Hananiya anayankha nati, Ambuye ndamva ndi ambiri za munthu uyu kuti anacitiradi coipa oyera mtima anu m'Yerusalemu;
14 ndi kuti pane ali nao ulamuliro wa kwa ansembe akulu wakumanga onse akuitana pa dzina lanu.