27 Ndipo ngati Ine ndimaturutsa ziwanda ndi mphamvu yace ya Beelzebule, ana anu amaziturutsa ndi mphamvu ya yani? cifukwa cace iwo adzakhala oweruza anu.
28 Koma ngati Ine ndimaturutsa ziwanda ndi mphamvu yace ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu.
29 Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m'banja la munthu wolimba, ndi kufunkha akatundu ace, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? ndipo pamenepo adzafunkha za m'banja lace.
30 Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.
31 Cifukwa cace ndinena kwa inu, Macimo onse, ndi zonena zonse zamwano, zidzakhululukidwa kwa anthu; koma camwano ca pa Mzimu Woyera sicidzakhululukidwa.
32 Ndipo amene ali yense anganenere Mwana wa munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma amene ali yense anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi yino kapena irinkudzayo.
33 Ukakoma mtengo, cipatso cace comwe cikoma; ukaipa mtengo, cipatso cace comwe ciipa; pakuti ndi cipatso cace mtengo udziwika.