4 Namuka Davide ndi Aisrayeli onse naye ku Yerusalemu, ndiwo Yebusi; ndipo Ayebusi nzika za m'dziko zinali komweko.
5 Ndipo nzika za m'Yebusi zinati kwa Davide, Sungalowe muno. Koma Davide analanda linga la Ziyoni, ndiwo mudzi wa Davide.
6 Nati Davide, Ali yense woyamba kukantha Ayebusi, yemweyo adzakhala mkulu ndi mtsogoleri. Nayamba kukwerako Yoabu mwana wa Zeruya, nakhala mkuru iyeyu.
7 Ndipo Davide anakhala m'lingamo; cifukwa cace analicha mudzi wa Davide.
8 Ndipo anamanga mudzi pozungulira pace, kuyambira ku Milo ndi pozungulira pace; ndi Yoabu anakonzanso potsala pa mudzi.
9 Ndipo Davide anakula-kulabe, pakuti Yehova wa makamu anali naye.
10 Akuru a amphamvu aja Davide anali nao akulimbika pamodzi naye m'ufumu wace, pamodzi ndi Aisrayeli onse, kumlonga ufumu, monga mwa mau a Yehova akunena za Israyeli, ndi awa.