17 Ndipo ici ncacing'ono pamaso panu, Mulungu, koma mwanena za nyumba ya mtumiki wanu nthawi yam'tsogolo ndithu, ndipo mwandiyesera ngati munthu womveka, Yehova Mulungu.
18 Anenenjinso Davide kwa Inu za ulemu wocitikira mtumiki wanu? pakuti mudziwa mtumiki wanu.
19 Yehova, cifukwa ca mtumiki wanu, ndi monga mwa mtima wanu, mwacita ukulu uwu wonse, kundidziwitsa zazikuru izi zonse.
20 Yehova, palibe wina wonga inu, palibenso Mulungu wina koma Inu; monga mwa zonse tazimva m'makutu mwathu.
21 Ndiwo ayani akunga anthu anu Israyeli, mtundu wa pa wokha wa pa dziko lapansi, amene Mulungu anakadziombolera mtundu wa anthu, kudzibukitsira dzina, mwa zazikuru ndi zoopsa, pakupitikitsa amitundu pamaso pa anthu anu amene munawaombola m'Aigupto?
22 Pakuti anthu anu Israyeli mudawayesa anthu anu anu kosatha; ndipo Inu, Yehova, munayamba kukhala Mulungu wao.
23 Ndipo tsopano, Yehova, akhazikike kosalekeza mau mudanenawa za mtumiki wanu, ndi za nyumba yace, nimucite monga mwanena.