2 Ndipo Natani anati kwa Davide, Mucite zonse ziri m'mtima mwanu; pakuti Mulungu ali nanu.
3 Ndipo usiku womwewo mau a Mulungu anadzera Natani, ndi kuti,
4 Kauze Davide mtumiki wanga, Atero Yehova, Usandimangire nyumba yokhalamo;
5 pakuti sindinakhala m'nyumba kuyambira tsiku tija ndinakwera naye Israyeli, kufikira lero Gno; koma wa m'hema m'hema Ine, ndi wa m'kacisi m'kacisi,
6 Pali ponse ndinayenda nao Aisrayeli onse ndinanena kodi mau ndi woweruza ali yense wa Israyeli, amene ndinamuuza adyetse anthu anga, ndi kuti, Mwalekeranji kundimangira nyumba yamikungudza?
7 Cifukwa cace tsono, uzitero naye mtumiki wanga Davide, Atero Ambuye wa makamu, Ndinakutenga kubusa potsata iwe nkhosa, kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Israyeli;
8 ndipo ndakhala ndi iwe kuli konse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndakubukitsira dzina lakunga dzina la akuru okhala padziko.