4 Ndipo Davide analanda magareta ace cikwi cimodzi, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; Davide anadula mitsita akavalo onse okoka magareta, koma anasungako ofikira magareta zana limodzi.
5 Ndipo Aaramu a ku Damasiko anadza kudzathandiza Hadarezeri mfumu ya Zoba; koma Davide anakantha Aaramu amuna zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.
6 Ndipo Davide anaika asilikari a boma m'Aramu wa Damasiko; ndi Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nazo mphatso, Ndipo Yehova anasunga Davide kuli konse anamukako.
7 Natenga Davide zikopa zagolidi zinali pa anyamata a Hadarezeri, nabwera nazo ku Yerusalemu.
8 Ndi ku Tibati, ndi ku Kuni, midzi ya Hadarezeri, Davide anatenga mkuwa wambiri, ndiwo umene Solomo anayenga nao thawale lamkuwa, ndi nsanamira, ndi zipangizo zamkuwa.
9 Ndipo pakumva Tou, mfumu ya ku Hamati, kuti Davide adakantha khamu lonse la Hadarezeri mfumu ya ku Zoba,
10 anatumiza Hadoramu mwana wace kwa Davide, kumlankhula ndi kumdalitsa, popeza adayambana ndi Hadarezeri, namkantha; pakuti Hadarezeri adacita nkhondo ndi Tou; ndipo anali nazo zipangizo za mitundu mitundu za golidi ndi siliva ndi mkuwa.