1 Pamenepo Satana anaukira Israyeli, nasonkhezera Davide awerenge Israyeli.
2 Ndipo Davide anati kwa Yoabu ndi kwa akuru a anthu, Kawerengeni Israyeli kuyambira ku Beereseba kufikira ku Dani; nimundibwezere mau, kuti ndidziwe ciwerengo cao.
3 Nati Yoabu, Yehova aonjezere pa anthu ace monga ali kazana; koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? nanga afuniranji cinthuci mbuyanga, adzaparamulitsa Israyeli bwanji?
4 Koma mau a mfumu anamlaka Yoabu. Naturuka Yoabu, nakayendayenda mwa Aisrayeli onse, nadza ku Yerusalemu.
5 Ndipo Yoabu anapereka kwa Davide ciwerengo ca anthu owerengedwa. Ndipo Aisrayeli onse anali zikwi mazana khumi ndi limodzi osolola lupanga, ndi Yuda anali zikwi mazana anai mphambu makumi asanu ndi awiri akusolola lupanga,