1 Ndipo Davide anati, Pano padzakhala nyumba ya Yehova Mulungu, ndi pano padzakhala guwa la nsembe yopsereza la Israyeli.
2 Ndipo Davide anati asonkhanitse alendo okhala m'dziko la Israyeli; iye naika osema miyala afukule miyala, aiseme kuti amange nayo nyumba ya Mulungu.
3 Nakonzeratu Davide citsulo cocuruka ca misomali ya ku zitseko za zipata, ndi ya kuphatikizitsa; ndi mkuwa wocuruka wosauyesa kulemera kwace;
4 ndi mitengo yamikungudza yosaiwerenga; pakuti Asidoni ndi Aturo anabwera nayo kwa Davide mitengo yamikungudza yocuruka,
5 Ndipo Davide anati, Solomo mwana wanga ndiye mnyamata ndi wosakwima, ndi nyumba imene adzaimangira Yehova ikhale yaikuru yopambana, yomveka ndi ya ulemerero mwa maiko onse; ndiikonzeretu mirimo. Momwemo Davide anakonzeratu mocuruka asanamwalire.
6 Pamenepo iye anaitana Solomo mwana wace, namlangiza ammangire Yehova Mulungu wa Israyeli nyumba.
7 Ndipo Davide anati kwa Solomo mwana wace, Kunena za ine, kumtima kwanga kudati, ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba.