6 Onsewa anawalangiza ndi atate wao ayimbe m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, zisakasa ndi azeze; atumikire nazo m'nyumba ya Mulungu; ndipo Asafu, Yedutuni, ndi Hemani, anawalangiza ndi mfumu.
7 Ndipo ciwerengo cao, pamodzi ndi abale ao ophunzitsidwa ayimbire Yehova, onse anthetemya, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu.
8 Ndipo anacita maere pa udikiro wao, analingana onse, ang'ono ndi akuru, mphunzitsi ndi wophunzira.
9 Maere oyamba tsono anagwera a banja la Asafu ndiye Yosefe; waciwiri Gedaliya, iye ndi abale ace, ndi ana ace khumi ndi awiri;
10 wacitatu Zakuri, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
11 wacinai Izri, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
12 wacisanu Netaniya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;