21 wa pfuko la Manase logawika pakati m'Gileadi, Ido mwana wa Zekariya; wa Benjamini, Yasiyeli mwana wa Abineri;
22 wa Dani, Azareli mwana wa Yerohamu. Awa ndi akazembe a mapfuko a Israyeli.
23 Koma Davide sanawerenga iwo a zaka makumi awiri ndi ocepapo, pakuti Yehova adati kuti adzacurukitsa Israyeli ngati nyenyezi za kuthambo.
24 Yoabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga, koma sanatsiriza; ndi mkwiyo unagwera Israyeli cifukwa ca ici, ndipo ciwerengo cao sicinalembedwa m'buku la mbiri ya mfumu Davide.
25 Ndipo woyang'anira cuma ca mfumu ndiye Azimaveti mwana wa Adiyeli, ndi woyang'anira wa cuma ca m'minda, m'mizinda ndi m'miraga, ndi nyumba za nsanja, ndiye Yonatani mwana wa Uziya;
26 ndi woyang'anira iwo akugwira nchito ya m'munda yakulima nthaka ndiye Ezri mwana wa Kelubi;
27 ndi woyang'anira minda yamphesa ndiye Simeyi Mramati; ndi woyang'anira zipatso za minda yamphesa zisungike mosungiramo vinyo ndiye Zabidi Msifimi;