25 Ndipo woyang'anira cuma ca mfumu ndiye Azimaveti mwana wa Adiyeli, ndi woyang'anira wa cuma ca m'minda, m'mizinda ndi m'miraga, ndi nyumba za nsanja, ndiye Yonatani mwana wa Uziya;
26 ndi woyang'anira iwo akugwira nchito ya m'munda yakulima nthaka ndiye Ezri mwana wa Kelubi;
27 ndi woyang'anira minda yamphesa ndiye Simeyi Mramati; ndi woyang'anira zipatso za minda yamphesa zisungike mosungiramo vinyo ndiye Zabidi Msifimi;
28 ndi woyang'anira mitengo yaazitona, ndi yamikuyu yokhala kuzidikha kunsi, ndiye Baala Hanani Mgederi; ndi woyang'anira zosungiramo mafuta ndiye Yoasi;
29 ndi woyang'anira ng'ombe zakudya m'Saroni ndiye Sitirai Msaroni; ndi woyang'anira ng'ombe za m'zigwa ndiye Safabi mwana wa Adilai;
30 ndi woyang'anira ngamira ndiye Obili M-israyeli; ndi woyang'anira aburu ndiye Yedeya Mmeronoti;
31 ndi woyang'anira zoweta zazing'ono ndiye Yazizi Mhagiri, Onsewa ndiwo akuru a zolemera zace za Davide.