18 Ana a Rubeni, ndi a Gadi, ndi limodzi la magawo awiri a pfuko la Manase, ngwazi, amuna akugwira cikopa ndi lupanga, ndi kuponya mibvi, ozerewera nkhondo, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zinai mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi limodzi akuturuka kunkhondo.
19 Ndipo anagwirana nkhondo ndi Ahagari, ndi Yet uri, ndi Nafisi, ndi Nodabu.
20 Ndipo anathandizidwa polimbana nao; ndi Ahagari anaperekedwa m'dzanja lao, ndi onse anali nao; pakuti anapfuulira kwa Mulungu pomenyana nao, ndipo anapembedzeka nao, popeza anamkhulupirira iye.
21 Ndipo analanda zoweta zao, ngamila zao zikwi makumi asanu, ndi nkhosa zikwi mazana awiri ndi makumi asanu, ndi aburu zikwi ziwiri, ndi amuna zikwi zana limodzi.
22 Pakuti adagwa, nafa ambiri, popeza nkhondoyi nja Mulungu. Ndipo anakhala m'malo mwao mpaka anatengedwa ndende.
23 Ndi ana a limodzi la magawo awiri a pfuko la Manase anakhala m'dziko; anacuruka kuyambira Basana kufikira Baala Herimoni, ndi Seniri, ndi phiri la Herimoni.
24 Ndipo akuru a nyumba za makolo ao ndi awa: Eferi, ndi lsi, ndi Elieli, ndi Azrieli, ndi Yeremiya, ndi Hodaviya, ndi Yadieli, anthu amphamvu ndithu, anthu omveka, akulu a nyumba za makolo ao.